Psalms 101

Salimo la Davide.

1Ndidzayimba za chikondi ndi chiweruzo chanu cholungama;
kwa Inu Yehova ndidzayimba matamando.
2Ndidzatsata njira yolungama;
nanga mudzabwera liti kwa ine?

Ndidzayenda mʼnyumba mwanga
ndi mtima wosalakwa.
3Sindidzayika chinthu chilichonse choyipa
pamaso panga.

Ine ndimadana ndi zochita za anthu opanda chikhulupiriro;
iwo sadzadziphatika kwa ine.
4Anthu a mtima wokhota adzakhala kutali ndi ine;
ine sindidzalola choyipa chilichonse kulowa mwa ine.

5Aliyense wosinjirira mnansi wake mseri
ameneyo ndidzamuletsa;
aliyense amene ali ndi maso amwano ndi mtima wodzikuza,
ameneyo sindidzamulekerera.

6Maso anga adzakhala pa okhulupirika mʼdziko,
kuti akhale pamodzi ndi ine;
iye amene mayendedwe ake ndi wosalakwa
adzanditumikira.

7Aliyense wochita chinyengo
sadzakhala mʼnyumba mwanga.
Aliyense woyankhula mwachinyengo
sadzayima pamaso panga.

8Mmawa uliwonse ndidzatontholetsa anthu
onse oyipa mʼdziko;
ndidzachotsa aliyense wochita zoyipa
mu mzinda wa Yehova.
Copyright information for NyaCCL